Pomwe anthu a chipembedzo cha chi_khristu akusangalalila kubadwa kwa Yesu pa 25 December, mpingo wa Zambezi Evangelical Church (ZEC) wapempha a Malawi kuti apewe zoipa pa nyengoyi.
Polankhula ndi Angaliba wachiwiri wa mlembi wamkulu wa mpingowu Reverend Innocent Mlelele Wachimwa wati zambiri zimakhala zikuchitika mu mdzina la chisangalalo koma zina sizikhala zolingana ndi zimene zimafunikira pa tsiku la Khrismasi.
Iwo anati ena amatenga mwayi wa tsikuli kuchita zoipa monga ndeu,kuledzera, chiwerewere ndi kuba kungotchula zochepa chabe zomwe anati mzolakwika.
“Iyi ndi nthawi yowonetserana chikondi pakuti Yesu anabwera kudzakhala Chikondi pakati pathu” Anatelo a Reverend Wachimwa.
Chomcho iwo amema a Malawi kuti patsikuli awonetsetse kuti asangalale moyenera.
Malingana ndi Reverend Wachimwa, Patsikuli anthu ampingo wa Zambezi Evangelical amakhala a kupemphera mmipingo yawo yomwe ikupezeka mzigao zonse za dziko la Malawi komaso maiko akunja.