Bungwe la FAM lasankha Patrick Mabedi ngati mphunzitsi wamkulu wa team ya Flames pa contract ya zaka ziwiri.
Chiganizochi chadza kutsatila mkumano omwe komiti ya bungwe la FAM inachititsa loweruka pa 22 October 2023, m’boma la Mangochi.
A Mabedi akuyembekezeka kuyamba ntchitoyi pa 1 November Chaka chino.
Wolemba: Elina Chitulu