Mkhalapampando wa mkhonsolo ya boma la Mangochi Hassan Chikuta wapempha anthu a dela la mfumu Chindongo ku Malindi m’boma la Mangochi kuti akhale ndi mtima wa umwini osamalila zitukuko zimene alinazo.
Chikuta walankhula izi Loweluka pa 23 September ,2023 pa mwambo otsekulila ogulitsila malonda ku delari.
Chikuta anati boma likupereka zitukuko zokhanzikika komabe ndi undindo wa eni ake kusamaliza zitukukozo.
Iye anati zimakhala zovetsa chisoni kuona anthu akulephera udindo wosamalila zinthu zamdera lao koma zikaonongeka amavutikaso ndi iwo eniake.
“Tiyeni tisamalile zinthu zimene tilinazo chifukwa ena akuzisowa.Ndipemphe adindo kuti pakhazikitsidwe komiti ya mphamvu yoonetsetsa kuti malowa akusamalidwa”.Anatelo Chikuta.
Polankhula ndi Angaliba utatha mwambowu Group Village Headman Chindongo anathokoza boma powaganizira ndi zitukukozo ku derali.Iwo anatchulaso za nyumba za apolice zimene zinatsekulidwa kale ndi mtsogoleli wadziko lino Dr Lazarus Chakwera kuti zabweretsa kusintha kuderali.Mfumuyi inalonjeza kuti awonetsetsa kuti msikawu ukusamalidwa moyenera.
Msikawu umene unamangidwa ndi Kampani ya zomangamanga yotchedwa Southgate construction yatenga ndalama zokwana K54,993,678.43 zomwe ndi za chitukuko zimene zimaperekedwa ku mkhonsolo.
Wolemba Blessings kaimira.(Mangochi).