Boma kudzera mu unduna wake wa zachuma wati laika ndondomeko zofuna kuchepetsa mavuto kutsatira kugwa mphanvu kwa ndalama ya Malawi.
Izi zanenedwa ndi nduna muundunau a Simplex Chithyola Banda ku Bingu International Convention Centre mu mzinda wa Lilongwe kudzera pa msonkhano wa atolankhani.
Zina mwa izo boma liyamba kupereka ndalama yokwana K50,000 pamwezi kwa anthu ocholera mabanja 184,920 omwe anakhudzika ndi Cyclone freddy mmaboma 9.Bomalinso lakweza chiwerengero cha anthu olandira mtukula pakhomo kuchoka 2 million kufika 3 million.Laikanso ndondomeko yoika pa mtukula pakhomo anthu ammatauni mabanja okwana 105 thousand omwe azilandira K150,000 pa mwezi.
Pa nkhani ya ntchito ndunayi yati akukambirana ndi mabungwe owona za ntchito kuti akweze malipilo.Ananenaso kuti boma lilemba azachipatala okwana 2741 ndiponso likulumikizana ndi maiko ena kuti boma lizitumiza anthu pafupifupi 5000 kukagwira ntchito kunja.
A Chithyola Banda anachenjezanso kuti boma lakhwimitsa chitetezo pamalonda a ndalama za kunja ndipo likwidzinga aliyese ochita malonda a ndalama za kunja mosatsata malamulo.
Msonkhano wa atolankhaniwu umene sunapereke mwai kwa atolankhani kufusa mafunso unadza kutsatira kugwa mphanvu kwa ndalama ya Malawi sabata yapitayi ndi 44 percent.
Kugwa kwandalamaku kwapangitsa kuti zinthu zambiri zikwere mitengo.Komabe boma linati ngati njira yothana ndi mavuto azachuma njira yabwino inali kugwetsa mphanvu ya ndalamayi ndipo anatsimikiza kuti posachedwapa zinthu ziyenda bwino.
Wolemba;Blessings Kaimira.