Ngati njira imodzi yopititsa patsogolo ntchito yopereka madzi aukhondo m’boma la Mangochi bungwe lotchedwa Evedence Action likugwira ntchito yoika mankhwala a Chlorine mmijingo.
Poyendera ntchitoyi mdera la Namiyasi lowelukali wachiwiri wa nduna ya zaumoyo Halima Daudi wayamikira ntchitoyi kunena kuti ikuthandiza kulimbana ndi matenda otsekula mmimba omwe amavuta m’bomali.
Polankhula ndi Angaliba Daudi anati izi zikuthandiza kuti anthu azimwa madzi otetezeka zomwe zipititse patsogolo thanzi lao.
Mmodzi mwa anthu omwe akupindula ndi ntchitoyi Magret Ajidu anathokoza adindo powaganizira ndi ndondomekoyi yomwe anati ikupindulila anthu ochuluka omwe amagwiritsa ntchito mijigo.
Padakali pano Evidence Action ikugwira ntchitoyi mmaboma 8 mdziko muno ndipo bungweri lakwanitsa kale kuika makina otulutsa chlorine opitilila 16,000.
Wolemba; Blessings Kaimira. (Mangochi)