Mwambo wa chaka chino wa Chiwanja cha Yao wayamba pa stadium ya Mangochi.
Mwambowu umene ukuchitika pa mutu oti kulimbikitsa chikhalidwe waitana anthu amtundu wa chiyao mdziko muno.
Mulendo olemekezeka ndi mfumu yaikulu ya chiyao Paramount chief kawinga.Atafika pamalopa mfumuyi anayendera zina mwa zinthu zomwe ayao amachita monga zakudya, Zovala,magule ndi chilankhulo.
Pamalopa palinso anthu ena odziwika monga Amida Mia amene waimira nduna yoona maboma ang’ono,second deputy speaker wa nyumba ya Malamulo Aisha Adams,Atupere Muluzi amene ndi mtsogoleri wakale wa chipani cha UDF,Mai Lilian Patelo amene ndi mtsogoleri wa chipani cha UDF,akulu akulu achipani cha DPP Bright Nsaka ndi Joseph Mwanamveka.
Wolemba;Blessings Kaimira.(Mangochi)
