Yemwe akuzaima nawo pa chisankho cha mchaka chamawa ngati phungu wa chipani cha Democratic Progressive Party ku Mulanje Limbuli Constituency a Daudi chida alonjeza kuti abwelaso mchaka chamawa kuzaikanso ndalama zankhaninkhani pa masewero osiyanasiyana kwa Achinyamata monga: mpira wamiyendo Kwa anyamata, mpira wamiyendo koma osewela ake mkukhala asungwana komaso mpira wamanja.
Achida amalankhula izi lamulungu masana pa bwalo la manyamba pomwe amagawa mphoto mu mpikisano otchedwa Daud Chida trophy.
Patsikuli panasonkhana anthu osiyanasiyana omwe anazachitila umboni za masewelo apaubale pakati pa Manyamba FC komanso Muloza select omwe unathera pofanana mphamvu pogolesana zigoli ziwiri kwa ziwiri.
Polankhula kwa atolankhani patsikuli a Chida ati ndikhumbo lawo kutukula masewero ku Mulanje kudzera ku mipikisano yawo yomwe iwo akukhazikisa pomwe zipaso zayamba kuoneka kale pomwe matimu monga Bangwe womens ikufuna osewela kuchokera kumatimu akuderali.